﻿EZARA.
2.
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 
Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere: 
Zidzukulu za Parosi 2,172 
zidzukulu za Sefatiya 372 
zidzukulu za Ara 775 
zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) 2,812 
zidzukulu za Elamu 1,254 
zidzukulu za Zatu 945 
zidzukulu za Zakai 760 
zidzukulu za Bani 642 
zidzukulu za Bebai 623 
zidzukulu za Azigadi 1,222 
zidzukulu za Adonikamu 666 
zidzukulu za Bigivai 2,056 
zidzukulu za Adini 454 
zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98 
zidzukulu za Bezayi 323 
zidzukulu za Yora 112 
zidzukulu za Hasumu 223 
zidzukulu za Gibari 95. 
Anthu a ku Betelehemu 123 
Anthu aamuna a ku Netofa 56 
Anthu aamuna a ku Anatoti 128 
Anthu aamuna a ku Azimaveti 42 
Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti 743 
Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba 621 
Anthu aamuna a ku Mikimasi 122 
Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai 223 
Anthu aamuna a ku Nebo 52 
Anthu aamuna a ku Magaibisi 156 
Anthu aamuna a ku Elamu wina 1,254 
Anthu aamuna a ku Harimu 320 
Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono 725 
Anthu aamuna a ku Yeriko 345 
Anthu aamuna a ku Sena 3,630. 
Ansembe anali awa:    Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) 973 
Zidzukulu za Imeri 1,052 
Zidzukulu za Pasuri 1,247 
Zidzukulu za Harimu 1,017. 
Alevi anali awa:    Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) 74. 
Anthu oyimba nyimbo anali awa:    Zidzukulu za Asafu 128. 
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:    Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai 139. 
Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za    Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, 
zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, 
zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, 
zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, 
zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, 
zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, 
zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, 
zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, 
zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, 
zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, 
zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, 
zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. 
Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu za    Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, 
zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, 
zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,    zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. 
Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali 392. 
Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi: 
Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali 652. 
Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za    Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) 
Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 
Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu. 
Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 
kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 
Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 
ngamira 435 ndi abulu 6,720. 
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 
Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100. 
Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo. 
