﻿NEHEMIYA.
7.
Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 
Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 
Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.” 
Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 
Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo: 
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 
Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere: 
Zidzukulu za Parosi 2,172 
Zidzukulu za Sefatiya 372 
Zidzukulu za Ara 652 
Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,818 
Zidzukulu za Elamu 1,254 
Zidzukulu za Zatu 845 
Zidzukulu za Zakai 760 
Zidzukulu za Binuyi 648 
Zidzukulu za Bebai 628 
Zidzukulu za Azigadi 2,322 
Zidzukulu za Adonikamu 667 
Zidzukulu za Abigivai 2,067 
Zidzukulu za Adini 655 
Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98 
Zidzukulu za Hasumu 328 
Zidzukulu za Bezayi 324 
Zidzukulu za Harifu 112 
Zidzukulu za Gibiyoni 95. 
Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa 188 
Anthu a ku Anatoti 128 
Anthu a ku Beti-Azimaveti 42 
Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 743 
Anthu a ku Rama ndi Geba 621 
Anthu a ku Mikimasi 122 
Anthu a ku Beteli ndi Ai 123 
Anthu a ku Nebo winayo 52 
Ana a Elamu wina 1,254 
Zidzukulu za Harimu 320 
Zidzukulu za Yeriko 345 
Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono 721 
Zidzukulu za Senaya 3,930. 
Ansembe anali awa: A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 973 
Zidzukulu za Imeri 1,052 
Zidzukulu za Pasi-Huri 1,247 
Zidzukulu za Harimu 1,017. 
Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74. 
Anthu oyimba:    Zidzukulu za Asafu 148. 
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za    Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai 138. 
Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za    Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, 
Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni 
Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi, 
Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, 
Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda, 
Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya, 
Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu, 
Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, 
Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, 
Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema 
Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa. 
Zidzukulu za antchito a Solomoni: Zidzukulu za    Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida 
zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, 
zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu    zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni. 
Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392. 
Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi. 
Zidzukulu za    Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642. 
Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo). 
Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 
Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu. 
Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 
Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 
Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 
Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720. 
Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 
Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 
Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67. 
Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo. 
