﻿MASALIMO.
2.
Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? 
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo. 
Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.” 
Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo. 
Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti, 
“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” 
Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako. 
Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako. 
Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.” 
Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi. 
Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera. 
Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye. 
