﻿MASALIMO.
12.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu. 
Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo. 
Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo ndi pakamwa paliponse podzikuza. 
Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu; pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?” 
“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.” 
Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri. 
Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya. 
Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo. 
