﻿MASALIMO.
82.
Salimo la Asafu. Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.” 
“Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa? 
Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. 
Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. 
“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. 
“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’ 
Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.” 
Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu. 
