﻿MASALIMO.
87.
Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; 
Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo. 
Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela 
“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ” 
Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.” 
Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela 
Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.” 
