﻿MASALIMO.
93.
Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe. 
Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya. 
Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo. 
Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, Yehova mmwamba ndi wamphamvu. 
Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; chiyero chimakongoletsa nyumba yanu mpaka muyaya. 
