﻿MASALIMO.
99.
Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke. 
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova; Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu. 
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri, Iye ndi woyera. 
Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera; mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo. 
Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera. 
Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha. 
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa. 
Inu Yehova Mulungu wathu, munawayankha iwo; Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka, ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa. 
Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mumulambire pa phiri lake loyera, pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera. 
