﻿MASALIMO.
100.
Salimo. Nyimbo yothokoza. Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. 
Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. 
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake. 
Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. 
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado. 
