﻿MASALIMO.
111.
Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano. 
Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira. 
Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 
Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo. 
Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya. 
Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina. 
Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika. 
Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama. 
Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa. 
Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya. 
