﻿MASALIMO.
117.
Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse; mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu. 
Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu, ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha. Tamandani Yehova. 
