﻿MASALIMO.
121.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? 
Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. 
Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera. 
Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona. 
Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja. 
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku. 
Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. 
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya. 
