﻿MASALIMO.
124.
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli, 
akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo, 
iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo; 
chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola, 
madzi a mkokomo akanatikokolola. 
Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. 
Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. 
Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. 
