﻿MASALIMO.
128.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. 
Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako. 
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. 
Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova. 
Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, 
ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli. 
