﻿MASALIMO.
129.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli; 
“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane. 
Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali: 
Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” 
Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi. 
Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule; 
sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo. 
Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.” 
