﻿MASALIMO.
149.
Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. 
Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. 
Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. 
Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. 
Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. 
Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, 
kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse, 
kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, 
kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova. 
