﻿YESAYA.
12.
Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati: “Ndikukuyamikani, Inu Yehova; chifukwa ngakhale munandipsera mtima, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mwanditonthoza. 
Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga; ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.” 
Mudzakondwera popeza Yehova ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu. 
Tsiku limenelo mudzati: “Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. 
Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu; zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi. 
Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.” 
